Waponda mwala namwali uja
Zomwe akupanga mmm wanga mutu waima
Momwe akuyendera timva pompano kuti waima
Poti aliyese mamuna angamuimitse umuona waima
Waponda mwala apo sindukaikira
Poti zaine saganizako
Lamya saimbako kapena uthenga kutumako
Kumugunsa palibe chanzeru amayankha
Kupita kwawo amati ndiotanganidwa
Kumuuza zochita amangoti akhala otanganidwa
Akufuna ngati Chiuta ndimpembetse?
Aaa kaya koma waponda mwala ndithu