Waitha wampatsa pathupi mtsikanayu
Ankanyada ngati Mfumu kazi iyeyu
Inde sitimamwa madzi chifukwa Cha iyeyu
Waitha wamuvalika chikweza iyeyu
Waitha waikanaso mimbayo
Poti malangizo ankawataira kumbuyo
Nawo mapempho achikondi ankakana
Ankatithawa ngati ndife asatana
Waitha wampatsa madzi amoyo
Ankaona ngati kupanda iyeyu sitikhala ndi moyo
Tikamadutsa kwawo ankatiseka
Apa nane mwachikhakhali ndizimuseka