Unali wanga zione
Cholichose ndimapanga kuti chikondi kwaiwe ndikupanga
Nthawi zonse palipose ndimakhala ndiiwe
Nyengo iliyose pa chilichose ndimakhala nawe
Koma zonsezi zinaphula palibe poti wachikondi pano ndilibe
Unali wanga wanga amadziwaso anzanga
Kumbuka Zione zomwe iwe ndiine tapanga
Mokunyadira ndinkukutchula kuti akazi anga
Koma kundisiya ndekha padzuwa ndi zomwe wasankha kupanga
Unali wapamtima wanga Zione
Kwa ena ngati Kalulu kwa galu ndinali m’dani chifukwa Cha iwe
Ndimalora kuthawa anzanga kuti ndisangalatse iwe
Inde,kuyesetsa kukukonda iwe
Koma palumbe kundisiya, Moti izi ndi mbiri chabe unali wanga Zione