Mkazi wanga Pede chilungamo ndiuze
Ngati pathupi ulinapo ndi panga
Poti sindikumvetsa zomwe ukupanga
Ndiwe mkazi wanga kapena wa mnzanga?
Pede yankhula zoona ngati ndilipo ndekha
Ukutha masiku ambiri kunja ine ndili ndekha
Kumapita kukajowa ziimbilo ine ndili ndekha
Yankhule Pede sindikufuna kudzidabwitsa ndekha
Pede duwa langa iwe
Kodi alipo angati othilira duwa iwe?
Dzulo ndakupeza ndi mphongo yakwa Chiphazi
Lero kukupeza ndi Wina wakwa Nthazi