Namwaliyo ndi chiphadzuwa
Amawala ngakhale Ali padzuwa
Ndithu dzulo loseli iyeyo ndi duwa
Pa iyeyo ndipo ndathera
Chiphadzuwa Nangondo wanga
Ndi mkazi owala Kwambiri Kwambiri
Nchifukwa chake ndimamukonda Kwambiri
Akazi enawa akuchepa kutali
Nchiphadzuwa chakudya changachi
Uyu yekha ofunika ndipite nayo ku Mangochi
Zodzola izi iye ai ndiwachilengedwe
Kumayamikira choterechi chilengedwe