Bola wakale uja
Aaa wabwino ndi uja ndinataya uja
Iwe chikondi chako chikondi nchowawitsa mutu
Poti nthawi ndi zako zochita umandiwawitsa mutu
Bola wakale uja
Poti zochita amamasuka komanso osasusuka
Iwe sumasuka komanso ndiwe osusuka
Zinthu sugawa ndiwe osuka
Bola wakale uja chiphadzuwa
Iwe suwala ngakhale litalowa mmitambo dzuwa
Chikondi chako chochita kupembedza
Ndakusiya poti ine munthu sindipembedza