“Pano!.., pano!.., mnyamata iwe!, iwe mnsungwana iwe!, uwu nkhwani wa nthete uwu, otchipa uwu, tabwera ingoona, bwera ndithu, ndikutchipisila”. Uku kunali kuyankhula moyitanila malonda kwa mnyamata wina dzina lake Mavuto. Mavuto m’nthawiyi amagulitsa nkhwani ku msika wina woyandikana ndi mmudzi wa kwawo. Mnyamatayi sukulu inamukanika kamba kosowa zozienereza pakuti kwawo kunali kosauka kwambiri kuphatikizila apo munthu amene anakatha kumuphunzitsa amene anali bambo ake anali atatsamaya.

Banja la kwa mnyamatayi anabadwamo ana atatu koma awiri anatsikila kuli chete mzilumika zingapo zapitazo ndipo mwana anasalamo yekha kotera iye amakhala ndi mayi ake. Kamba kosowa kangachepe iye anaganiza zomagulitsa nkhwani ndicholinga choti azithandiza pakhomo pakwawo paja. Mwachidule ndi momvetsetseka tinganene kuti Mavuto anauvala udindo wa ubambo tsopano.

Ngakhale iye pamodzi ndi mayi ake amayesa kuthamangathamanga zinthu sizinalibe kusintha, limati vuto ili likamatha lina limalowa m’bwalo. Kunenetsa zimangokhala ngati anthuwa ali m’dzenje la mavuto.

Patapita zaka zingapo mayi ake a Mavuto anatsamila dzanja. Zoterezi zinapangitsa kuti mwana wa mphongo abalalike kwambiri. Zinthu zinafika poipa popeza mnyamatayi akapita mwa azibale pofuna thandizo lawo amamupitikitsa ngati nyani oba mtedza. Moyo omangopanga zake unadzika midzu mmalingaliro mwake kotero anayamba kumapanga timaganyu tosiyanasiyana ndicholinga chofuna kumazithandiza yekha. Thupi la mavuto linazilala, ankavala sanza zokhazokha, malondi katundu wa kwawo azibale anagawana ndipo iye analibe kokhala kulikonse kotero amangogona paliponsepo pamene papezeka tsiku limenero. Kunenetsa mnyamatayi ankamvetsa chisoni kwambiri.

Tsiku lina Mavuto akuziyendera anaona mtsikana wina atasenza chikwama. Kwa iye uwu anauona ngati mwayi oti apempheko ganyu yonyamula chikwamacho ndipo anasatila munthuyo namuimitsa.

“wawa che…chemwali, ndingakuthandizeniko kunyamula chikwamachi?” Anapempha mozikolakola ndi mwachisoni mwana wa m’muna. “Ayi ndithu musadandaule ndinyamula ndithu”. Anayankha motero mntsungwanayo uko akupitiliza ulendo wake. Apa mavuto sanaimve koma kuthamangilabe mnamwaliyo. Anayesa kumupempha umu ndi umo koma zinalephereka mmalo mwake mnsungwanayo anangomutonza ndikumuyankhulira mawu a chipongwe amene iye anakhudzika nawo kwambiri koma sanadandaule popeza anali atangofika pozolowera kutonzedwa.

Njala inamuwawa kwambiri Mavuto koma kanthu koti aponye mmimba samkakaona. Ali mu nkhalango yolingalira za umo mmene angapezere chakudya anaona mkulu wina ali ndi muthu wa mayi mgalimoto ina akudya mpunga ophikidwa mwa luso. Ganizo loti apempheko chakudyacho linamubwerera ndipo anatsendera pafupi. “Wawa-wawa”. Anayamba kuyankhula motero Mavuto. “Wawa”. Anayankha anthuwa modabwa. “Pepani ndakusokonezani, ndimati ndipempheko ndithu, njala ikundiwawa munthune, mungandigaileko chakudyacho?”. Anayankhula mozichepesa Mavuto.

Ndi mawu awa bambo ndi mayiwa anayang’anizana koma mosaonesa kukhuzika kulikonse. Iwo amkangopitiliza macheza awo n’kumapsopsonana. Mnyamatayi atatopa n’kudikila anayankhula mopereka funso, “koma mwamva pempho langali?”Apa Mavuto anangokhala ngati wawathila chitedze kotero anangomuyankha za chipongwe zokhazokha. Apa mwana wa mphongo sanakachitila mwina koma kungochokapo misozi yonga mvula ikutsikila mmasaya mwake.

Tsikuli Mavuto anayesa njila zonse kuti apeze ka chakudya koma zinalephereka popeza njila iliyonse imene iye ankayesera ankalandila nayo chitonzo kotero ganizo lomangotoleza tizakudya linamubwerera. Zinthu zinafika poipa moti Mavuto ndi munthu waziwala mmaso samkasiyana tsopano. Ali mkati motoleza tizakudyato anaona kachikwama kena kake, anakatenga nakasunga ndikupanga ganizo loti akatsegulabe. Atafika malo ena obisika anatsekula ka chikwamako napezamo foni imene imaoneka kuti ndi ya ndalama za nkhaninkhani, chitupa choyendera ndi ma pepala osiyanasiyana amene kwa iye analibe phindu lililonse. Kotero iye anangochosamo foniyo chikwamacho ndikuchitaya.

Patatha sabata zingapo Mavuto anamangidwa ndikuponyedwa mundende pa mlandu opezeka ndi foni yobedwa ndi’nso kuti kumene inabedwako mwini wake anaphedwa.

Patatha miyezi ingapo Mavuto anatulusidwa m’ndende muja atapezeka kuti ndi osalakwa.

Moyo unafika povutitsitsa kwambiri tsopano. Mawu oti “zabwino zili mtsogolo” amkazungulira mmutu mwa mnyamatayi. Moyo odya zogenda unamutopetsa kotero ganizo losaka ka ganyu kokhazikika linam’bwerera ndipo ntchito yosakasaka kachochitako inayambika. Mavuto anasakasaka ntchito umu ndi umo koma sanaipeze mmalo mwake anthu olemba ntchitowo amangomuyankhulira za chipongwe ndikumubweza. Izi zinali chomwechi kamba ka maonekedwe ake ndinso poti analibe ma pepala aliwonse. Ngakhale Mavuto anali kutonzedwa chotero koma iye samagonja kotero analibe kusakasaka tizochitato.

Tsiku lina Mavuto akuziyendera uko akudya peyala lopsetsetsa limene analitola kwinaku atazipakapaka za mapeyalazo zovala zake zonse anatulukila malo ena olembera anthu ntchito. Apa iye anaona anthu ambiri ovala bwino ali zungulizunguli. Mavuto mozikaikila anaima nakhala poteropo. Anthu ambiri anamuyang’anitsitsa Mavuto. Sikunalitu kungoyang’ana wamba koma kuzazidwa ndi mafunso. Izo zinali chomcho potengera mmene anali kuonekera. “Ukuzatani kuno?” Ili linali funso limene iye munthawiyi ankalimva pafupifupi kuchokera kwa munthu aliyense amene anali pamalopo. Izi zinali chomwecho pakuti aliyense amkaganiza ngati mnyamatayo ndi waziwala mmaso ndipo anapitikisidwako.

Mavuto adakalibe mkati moziyendera adafika pa nseu wina waukulu. Akuti azioloka kupita mbali ina ya nsewuwo kulira kwa ma buleki kunamveka kuti kwichii!!, apa Mavuto anakagundidwa ndithu. Mosakhalisa mwini galimotoyo anatsika nayamba kumulalatila kwinaku akumutukwana kumene. Anthu ena amene analiso chapafupi anatsendera pofuna kuona ndinso kumva chimene chimachitika. Mavuto anayesa kufotokoza koma sizinaphule kanthu. Zimkachitikazi zimkamukhuza kwambiri kotero misozi yonga mvula inayamba kugwa kuchokera mmaso mwake. Kenaka iye anangochokapo uko akugwedeza mutu wake chammbali ngati uli ndi mnyanga.

Dzuwa linapendeka, Mavuto atatopa nako kuyenda anakhala pansi mphepete mwa nseu. Atangokhala anaona mdima mmaso mwake kenaka kunayera, njala ndi ludzu zinamuwawa kolapitsa. Iye analakalaka nthaka inakangong’ambika n’kumumeza. Ali chikhalire chomwecho anaona bambo wina wovala bwino akulowa mgalimoto mwake botolo lake la madzi lili mmanja. Bamboyo atangolowa mgalimotomo Mavuto anapita chapafupi napempha madzi. Bamboyo akupereka madzi aja mnyamatayo anagwa pansi. Zoterezi zinapereka mantha aakulu kwa mkuluyo.

Anthu ena amene anali chapafupi anatsendera pafupi. Bamboyo anawafotokozera zonse mmene zinakhalira ndipo anthuwo anamvetsa. Mavuto anatengedwera ku chipatala ndi bamboyo popeza munthawiyi anali ali chikomokore. Ku Chipatala kuja atamuyeza anapeza kuti gwero la matenda a mnyamatayo ndi nkhawa, kotero magazi ake adali kuthamanga mosaenera zimene zinapangitsa kuti ziwalo zotanthauzira mauthenga zisagwire bwino ntchito yake pathupi lake. Dotolo atawafunsa bambowo zambiri za mnyamatayo iwo anafotokoza momveka bwino lomwe kuti mnyamatayo samudziwa konse koma a dotolowo anawauza kuti zimenezo zilibe kanthu ndipo munthawiyo mnyamatayo amafunikira kwambiri thandizo lawo popeza analibe achibale aliwonse amene anali naye limozi munthawiyi. Zitatero bamboyo anauza dotolo uja kuti akubwera kaye ndipo dotoloyo mosakayika konse anavomereza podziwa kuti bamboyo abweradi popeza anali otchuka.

Bamboyo anauyatsa ulendo wa kwawo pa galimoto yake. Kunenetsa bamboyi anali mmodzi wa mponda makwacha a mdera lakwawo. Atafika ku nyumba kwawo kuja bamboyo anafotokozera banja lako za mnyamata uja. Pamapeto pa zonse bamboyo pamodzi ndi banja lake anagwirizana zokatenga mnyamata uja kuti amusamalire kwa kanthawi.

Chotchingira pa khomo la mpanda chinatsegulidwa ndipo galimoto linalowa mkati. Kunali bwalo ndithu, nyumba yaikulu yomangidwa mwa makono, maluwa onunkhila ulemerero ndi mitengo ya zipatso yochuluka. Maonekedwe akumaloku amaulura okha kuti kunali kwa mponda makwacha.

Mavuto anatengeredwa mnyumba nalandilidwa moziwisidwa kwa anthu onse a pakhomomo.

“ine ndine bambo Gerezani, mwini malo ano. Awa ndi akazanga okondedwa, mu banja lino muli mphatso ya ana awiri okha wamwamuna ndi wamkazi ali apayi ndipo wamwamunayo ndi uyo.” Anayankhula motero bambo Gerezani akumwetulira. “Msungwanayi dzina lake ndi Eliza ndipo mnyamatayi ndi Alani.” Anapitiliza kuyankhula bambo Gerezani akuwaloza anawo.

“Zikomo kwambiri nonse, ine ndi Mavuto” anatero Mavuto akutembenuza maso ake mopitisa uku ndi uko.

Mosakhalisa mayi Gerezani anafunsa mafunso okhuza kumene Mavuto amakhala ndi banja lakwawo ndipo iye anayankha mwachilungamo ndi mozichepesa. Zitatero anthuwa anadya mgonero kenaka Mavuto anapasidwa chipinda chake chogonamo ndipo kuchoka tsiku ili anali kukondedwa ngati mwana wa banja lomwelo.

Pakupita kwa nthawi Mavuto anapasidwa mwayi oti akayambe sukulu ya sekondale popeza anasiila folomu yoyamba ndipo zinathekadi. Mavuto anali kukhonza kochitisa chidwi. Nthawi zambiri iye amamuthandiza Alani ndi mchemwali wake zinthu za zukulu zikawavuta ngakhale awiriwa anali makalasi akutsogolo. Alani anali folomu yachinayi pamene Eliza anali folomu yachiwiri.

Mavuto anafika folomu yachinayi. Analemba mayeso ndipo anakhonza bwino dzedi. Anapezeredwa malo ku sukulu ya ukachenjede wa za udotolo koma iye anakana kupitako mmalo mwake anawapempha a Gerezani kuti amulore asate za maganizo ake ongophunzira ntchito yamanja yokhonza ma pampu opopera madzi. Anthu ambiri anamuseka pa chiganizo chimene iye anapanga koma pakupita kwa nthawi anayamba kumumvetsa bwino lomwe zomwe anapangazo zitayamba kubala zipatso.

Mavuto anayamba ntchito ya pamwamba kwambiri. Iye adali asanapeze kakumphatsa. Ntchitoyi sanaigwire kwa nthawi yaitali mmalo mwake anaisiya ndikumapanga za ulimi wa nthilira pogwilitsa ntchito ma pampu opopa madzi amakono ndipo zimamuyendera. Mozichepetsa ndi mozipatsa ulemu mnyumba mwa a Gerezani muja anachokamo nakayamba kukhala yekha. Anthuwa amkayenderana pafupipafupi. M’nthawiyi n’kuti Alani atapita kunja kwa dziko lino kukapitilizabe maphunziro ake a ukachenjede koma Eliza akukhalabe ndi makolo ake aja ndipo adali akuimbabe sukulu.

Nthawi zambiri Eliza amamuyendera Mavuto. Machezedwe a anthu awiriwa anali kusiyana ndi kale tsopano pakuti anali kuchitilana manyazi koposa. Kuonjezera apo ukabwerebwere wa mnamwaliyu pang’ono ndi pang’ono unayamba kuzimangira nyumba mmalingaliro mwa mnyamatayu. Tsiku lina mwa chizolowezi Eliza anabwera kwa Mavuto kuja. Awiriwa anacheza nkhani iyi ndi iyo kufikila nthawi yoti mnsungwanayo azipita inakwana ndipo Mavuto anamperekeza.

“Ndili ndi nkhani inayake Eliza, imene ukaimva iwusa mafunso ambiri mmutu mwako, mwa chiziwikire uwona ngati ndayamba kubalalika. Utha kuona ngati umunthu wanga wathawa, mutu wanga wasiya kugwira ntchito, komano ukuyenera kungondimvetsetsa ndi kuvomereza.” Anayamba kuyankula choncho Mavuto moonesa manyazi ndi mantha a mnanu.

Tsikuli Mavuto anayankhula mawu ambiri odzadza ndi chikondi. Muzoyankhula zake sizinali kuzungulira mmbali kwenikweni koma kulunjika pa mfundo yoti wamukondetsetsa mnamwaliyo. Eliza pakumva izi anakanitsitsa pomuuza kuti iyeyo ndi mchemwali wake koma Mavuto atanyengerera Eliza ndi timawu tofewa mwana wa mkazi anatheka, ndipo chibwezi cha awiriwa chinayambira pamenepa.

Chibwezi cha Mavuto ndi Eliza chinafika pa mponda chimera. Ngakhale izi zinali dere koma makolo a mnamwali aja samadziwa kalikonse.

Mazulo wa tsiku lina Eliza ali mkati mocheza ndi makolo ake aja muchipinda chochezeramo anawasina khutu makolo akewo kuti wapeza mwamuna amene amakondetsetsana naye. Iye adati mwamunayo wakhala naye pa chibwezi kwa kanthawi ndipo mkatikati mwa masiku angapo akubwerewo adza naye kuti azamuthire diso. Makolowo atamva izi anasangalala kwambiri popeza Eliza anali atafikadi mnsinkhu woti atha kukwatiwa pakuti sukulu anali atathana nayo tsopano ndipo anali akugwira ntchito. Pa tsikuli Eliza sanatchure kuti mwamuna wake ndi ndani.

Tsiku lina Mavuto cha kumasana anapita kwa a Gerezani kuja. Atafika anawapeza mayi Gerezani okha. Mavuto anayamba kucheza nawo nkhani iyi ndi iyo. Mosakhalisa mayi aja anayamba kufotokoza za mwamuna amene Eliza amati wapeza uja. Mavuto atamva za nkhaniyo sanafune kuziulula yekha kuti mwamuna amakambidwayo anali iye. Mmalo mwake anangoti “nkhani yosangalatsa, a Eliza akula tsopano”. Ali mkati mocheza chotero Eliza anatulukila. Adakali chichezere chotero a Gerezani anatulukilanso. Onseno pamodzi anayamba kucheza uku ali patebulo kudya ndi kumwera limozi. Mosapita nthawi bambo Gerezani anagunda nkhani ya Eliza ija. Nkhaniyo itatokosedwa mayi Gerezani anavomereza ndipo nkhaniyo amkasinthana mkamwa anali mayi ndi bambo okha. Mavuto anasanzika kuti akukataya madzi kaye. Awiriwa anamufunsaso mwana wawoyo za mwamuna amanenayo ndipo iye anangoti mwamunayo alipo ndipo abwera tsiku lomwero kuti amuziwe.

Mavuto anabwerako kotaya madzi kuja nakhala pansi. Amkaoneka wa mantha otsakanikilana ndi manyazi. Mwana wamwamuna anapezeka. Anakoka mpweya nautulusa motaiza. Mmalingaliro mwake anamangitsa mfundo yowaziwitsa makolowo kuti mwamuna amkanenedwayo anali iye. Ali mkalikiliki ofuna kuziulula kugogoda kunamveka pa chitseko. Uyu anali mmodzi wa anthu amene amapanga malonda ogula ndi kugulitsa mbewu zakumunda ndi bambo Gerezani. Mkambilano wawo ndi mlendoyo sunatenge nthawi kwenikweni. Mavuto anayamba kunjenjemera, misonzi inalengeza mmaso mwake ndipo thukuta linayamba kuyenderera pathupi lake. Zonsezi amkaziona anali Eliza.

”Makolo anga muli apa, ndimadziwa kuti ndinu anthu abwino, chonde ndikupempha kumvetsetsa kwanu. Musandikwiyire pa chilichonse chomwe mutanve pano. Ndikudziwa, musiku lalero muli ndi chidwi chofuna kudziwa mwamuna emwe mtima wanga unakonda. Ndichinthu chamanyazi kwambiri kwa ine pochedwa kukudziwitsani. Pakuti zinthu zaonongeka kale tingovomereza. Ndizapempha madalitso anu ndi kumulandira mwa chikondi munyumba ino pakuti ndi yekhayo amene mtima wanga unasankha ndipo palibeso wina ayi ndi yekhayo basi”. Eliza anayankhula motero moonetsa mantha uko misonzi ikuyamba kuyenderera mmasaya mwake.

Ndi mawu awa bambo ndi mayi Gerezani anayang’anizana kenaka analonjeza mwana wawoyo kuti azamulandira munthuyo ndi manja awiri m’banjamo.

Eliza anakhazikisa mtima tsopano ndipo anaulura kuti mwamunayo anali Mavuto.

“Timkaziwa kuti ngakhale titabisa mwa mtundu wanji muzadziwabe basi. Ndiye posafuna kukuchoselani ulemu ndi chifukwa chake tabwera mogonja pa maso panu kuzakudziwitsani tokha kupangira pa mawa. kunenetsa, zimene akunena Elizayi ndizo zoona zake. Ndinganene kuti pakadali pano Eliza ndiye mkazi wanga, chonde vomerezani pa ichi”. Anayankula chomwechi Mavuto mozichepesa.

Makolo atazukuta zoyankhula za anawa anazindikila kuti Eliza ndi oyembekezera kotero anakakamizika kuvomereza izi ngakhale kwa iwo zinali zochititsa manyazi.

Alani anadziwitsidwa za nkhaniyi ndipo nayeso sanakachitira mwina koma kuvomereza. Chisangalalo chinakuta nkhope ya aliyense chifukwa adali kudikira kuona mphatso ya mwana amene amayembekezera kuona dzikoli.

Nkhani ya M’MOYO UNO yathera pamenepa.