“Anditenga kusukulu ya ukachenjede, tumizani ndalama zambiri zoti ndikagwiritse ntchito kumeneko”, adatero Kanyenthe powuza abambo ake palamya. ” Nditumiza mwana wanga,ndikabwereke kaye kwa Kaigwa,” adayankha motero a Phiri.
Kanyenthe adali mwana wachisamba m’banja la bambo ndi mayi Phiri.Ali wachichepere Kanyenthe adali mwana womvera ndi waulemu. Zinthu zidasintha pomwe Kanyenthe adatumizidwa ku sukulu yogonera komweko ya Pops ali sitandade 6, Iye adayamba kusuta,kuba ndu kumwa mowa. Atalemba mayeso a sitandade 8 Kanyenthe akakhozera ku secondale yogonera komweko ya Mkanda. Atayamba sukulu yake pa sukulu ya Mkanda makhalidwe ake oioa sadasiye ngakhale kuti makolo ake sankadziwa zamakhalidwe ake oipawa. Atafika fomu foll adasiya kulipila sukulu fizi komanso adadya ndalama ya mayeso moti mayeso a MANEB sadalembe Kanyenthe adaganiza zopita kwa Kamwendo komwe ankakhalira umbava ndi umbanda.
Zotsatira zamayeso zitatuluka Kanyenthe adawauza makolo ake kuti iye wakhoza kuposa aliyese pa sukulu ya Mkanda ndipo amusankhira ku sukulu ya ukachenjede yotchedwa College of Medicine (COM).”Anditenga kusukulu ya ukachenjede tumizani ndalama zambiri zoti ndikagwiritse ntchito kumeneko,” adatero Kanyenthe powuza abambo ake palamya. Nditumiza mwana wanga ndikabwereke kaye kwa Kaigwa,” adayankha motero a Phiri. Kanyenthe adakhala akunamiza makolo ake kuti ali ku sukulu ya ukachenjede pomwe adali akukhala kwa Kamwendo. Tsiku lidakwana loti Kanyenthe adziwike. Lidali loweruka pomwe a Phiri adaganiza zokakoza chitupa chotumuzira fodya kwa Kamwendo. Atafika pamsika wanjala adazizwa khwimba la anthu likukuwa munthu wina theyala Lili mkhosi. “Aotchedwe Kanyenthe mbavayo” ,” lidatero fumbilo. A Phiri poonetsetsa adazizwa kuti mbava imafuna kuotchedwayo adali mwana wawo. A Phiri adali okhumudwa chifukwa adadziwa kuti mwana wawo ankawanamiza ndipo adali Kanyenthe.
The end