WADYA CHANI?
Wadya chan mwanawe?
Mimba yako yatani ? Tayankha mwanawe
Wayamba kuvala chikweza ukuti nchiyani?
Ukungogona mnyumba chanchitika nchiyani?
Mwanawe watani ? Masuka
Thupi lako lose ngati nchenga wakunyanja layela
Tinene kuti chouluka chatera?
Tayankha mwanawe paja anga malangizo udati mpaka kale sudzamvera
Pitaso koyendatu mwanawe
Paja umavala tawazaka ziwiri tizovala
Yankhula apa paja ndiwe ozala
Ndiyankhe mwanawe, wadya chani?