Usandifune lero mkazi

Kumbuka kuti ngati Yudas udandikana

Udakanitsitsa ngati ndine Satana

Pita uko nthawi ndilibe yotaitsana

Usandifune lero wonyada iwe

Kuti ndine wopanda ntchito udanena

Waona chan kuti undifune? tanena

Ndisiye ndikuti usandifune

Usandimwetulire poti lero zikuyenda

Moni usamandipatse ndi Nangozo pamsewu tikamayenda

Udandikana kale pano ndinapeza wina

Nawe choka usandiyandikire Satana