Ukadanena usadapite chiphadzuwa changa
Kuti umadana ndi masese ukadafotokoza mkazi wanga
Ndipo kuti wamkulu fodya udana naye ukadandiuza bulangete langa
Osati kungondisiya Siya ndekha ndekha pamphepo nditadekha
Taona ndangoti manja mkhosi gwire kusowa chochita ndekha ndekha
Ukanandiuza Kaye zomwe umadana nazo
Ona lero padzuwa ndekha ndekha ndikulimbana nazo
Ukadandiuza kuti zomangoswera pabawo umadana nazo
Taona zolakwa ine ,Viyezyo akuvutika nazo
Wandilakwira Nyagondwe poti ndi izi mtendere ndikusowa nazo
Ukadanena Kaye nthiti yanga
Kuti kuyankha mochedwa wako uthenga umadana nazo ukadandiuza
Ndipo kuti momasuka kucheza ndi anzako ai ukadandiuza
Ndikadasintha kale kale ine chifukwa ndimakukonda
Koma poti wanyamuka kale zabwino zonse ngakhale ndikadakukonda