Takumbuka namwaliwe
Ku Chiskemba pa Phiri ndili ndiiwe
Ukundigwira ngati mawa kulibe
Ukunenetsa kuti kusiyana iwe ndiine kulibe
Takumbuka chiphankhawa
Tili mu Lukali ukundichotsa nkhawa
Ndipo ukunena kuti ukakhala ndiine suda nkhawa
Nanga lero ukuti nazo bwanji?