Akaziwa osawakonda Kwambiri
Mudzakhumudwa nawo
Amakhala akuganiza zawo
Zaiwe sauzako anzawo kapena makolo awo
Akaziwa zomwe amafuna samadziwa
Zoti Ali ku ntchito Zina iwe sumadziwa
Inde zoti ukuwakonda Kwambiri samadziwa
Akaziwa osawakonda Kwambiri
Anthuwa ndiabweretsa ndikudyere
Ukadzipereka ngati msamaliya apanga zoti akudyere
Inetu ndakondapo, ndathawidwapo ndi kudyeredwapo
Nchifukwa ndikuti akaziwa osawakonda Kwambiri