Mwanawe kuti dzikoli lisadzakuwawe
Zinthu zoipa zadzikoli mwadala usazilawe
Bibida, jang’ala , hona ndi ambuye mtengeni usadzalawe
Poti ukatero ndeti ukufuna dzikoli kuwawa udzalimve
Mwanawe dekha dziko ndilomvuta
Anthu amdzikoli mmm ndiovuta
Zibwana dala usapange
Njuga ndi uhule chonde usamapange
Mwanawe usanyalanyaze anga malangizo
Nthawi zonse uzimvera abwino malangizo
Ndipo ukatero wadziko sudzauva ululu
Poti dzikoli ndi Chibwana ndi galu ndi kalulu