Ndine mtsikana wachimalawi.
Weni weni mmYao.
Uko ku Zomba ndichonena .
Dela la a TA kuntumanji kwa Kandulu.
Chitenje ndiye chovala chama.
Nawo mpango kumutu suchoka.
Zizindikilo zachikhalidwe changa.
Chikhalire chokoma ndipo chosangalatsa.
Nsondo, litiwo,Ndakula ndi jando.
Ndiye zina mwazikhwalidwe zathu.
Uko komwe kwa aYao.
Futali ,Mobile,Mpunga ndi Thobwa ndiye dzakudya wathu.
Mukamva “abiti” musadabwe nazo.
Ndinjila ina yolemelezela athu athu atsikana achiYao
Ndipo ndikunena,
Inde ndikunenetsa
Ine ndi mMalawi.
Une mwanache wachikongwe wachiYao.