Kaja katherere kachipande

Mudatibweretsera padzana paja

Ndithudi ubale wa konzunkozu ukomadi

Zoti ndinu anansi ndavomerezadi

Chathu chibale nchozimiranadi ndevu

Kuning’a pakati ngati chimvano chamavu

Mwainu ndithu ubwino ndauonadi

Wondithandiza ntchentche nditafundadi

Umodzi mutu denga susenzadi

Waife m’modzi mbonaona akaonadi

Akokoli avumbuluka nakuthawani

Koma ife titenga ubwino pokuthandizani

Ngati nyerere ifedi tiyenda

Zathu zinthu tiikadi mndandanda

Ubale wathu ukomadi nkuyenderana

Tikhalira pamodzi nthawizonse nkusangalala.