Iwe umati bwa?
Chamba chomwe umafuta umati uchita Cha?
Phindu lake ndi misala yomwei basi
Umati nzeru zichuluka chamba chomwechi basi?
Iwe umati bwa?
Uhule umapanga uja umati ndalama uzipeza
Ai phindu lake ndi matenda omwewa wapeza
Udabwa kuti ngati ndi ntchito osaipeza
Iwe umati bwa?
Kuba umaba umaona ngati uzidyera tsiku ndi tsiku ?
Zinthu zimasintha tsiku ndi tsiku
Ona akuotcha lero ndi zakale amangokusiya