Ndili mu ululu wa zaoneni.

Anga mabala akuthamangisa mtima.

Kupangisa mwazi kusempha msewu zache.

Nkhawa zazimangira nyumba pa thupi langa.

Ndimagwira tambala pakhosi tsiku ndi tsiku.

Kuyesesa kuti pakhomo pasakuwe agalu akuda.

Mmaso mwanga misonzi siilekedza.

Thupi langa lonse linamatidwa phula,

Potengera zilingo zomwe ndimachita.

Kodi kusaka mchere ndikulakwa?

Kuti ukabwerako mochedwa uzilandila mathokozo onga awa?

Chongoti mnyumba loweni, madzi a moto m’thupi lonse puu.

Mwati simundikankhizira kulichete akumphasa anganu?