“Bwerani, aliyense!” Tin anatero mokweza. “Tiyeni tisangalale! Kapena mukufuna We Can Band kuti ikuthandizeni?”

“Yebo, inde!” khamu la anthu linatero mokweza.

Tin anayang’ana-yang’ana pozungulira. “Gulu la woyimba lili kuti? Oo ayi, sindingawawone kulikonse. Si phwando ngati palibe oyimba. Ndikufuna thandizo lina. Gulu lokha ndi lomwe lingakwaniritse izi!” Tin anamwetulira akuyang’ana gulu la anthulo. “Poyamba, ndimafuna owomba ng’oma awiri.”

Neo ndi Hope ndi omwe adakweza manja awo poyamba. Atakwera pa siteji, Tin adawapatsa zitini zinayi za khofi zili ndi zivindikiro za pulasitiki. Zitinizo zinali zokongoletsedwa ndi pepala lowala kwambiri komanso mabatani. Panalinso timitengo ta ng’oma toti Neo ndi Hope azigwiritsa ntchito.

“Tsopano tikufuna ogwedeza mphonda,” adatero Tin.

“Josh! Sankhani Josh!” adatero Neo mokweza.

“Kodi Josh ali pano? Josh ali kuti? Tiyeni timubweretse kuno,” Tin anaseka.

Josh anakweza dzanja lake. Amuna awiri adakweza wilicheya yake pa siteji.

“Takulandirani, a Josh,” adatero Tin. “Yesani kugwiritsa ntchito mphondazi ziwiri.”

Josh adagwedezera imodzi kenako ina. Zinamveka mosiyana.

“Ndi zabwino kwambiri, adatero Tin. “TSOPANO, LOLANI …”

Koma asanamalize kunena, kunamveka phokoso lalikulu. Aliyense anayang’ana uku ndi uko kuti awone chinali choyambitsa phokosolo.

Kenako Noodle anathamangira kudutsa pa sitejipo, akukoka zitini zomangirizidwa pamodzi ndi chingwe kumbuyo kwake.

“Phokoso labwino!” Tin adatero mokweza. “Ndimaganiza kuti ndawataya.”

Bella anathamangira ku sitejiko. “Noodle!” adamuyitana. Noodle anathamangira komwe kunali ndi Bella, zitini zikugundana mwaphokoso kumbuyo kwake.

“Palibe vuto,” anatero Tin akuseka. “Ndikuganiza kuti Noodle akufuna kukhala membala wa We Can Band. Ndiyeno ndikuganiza kuti akufuna inunso kuti mugwire ntchito limodzi nafe,” anatero akuloza Bella.

Tin anathandizira Bella kukwera pa siteji ndiponso onse pamodzi adamasula zitini zomwe zinali zinamangiridwa pathupi la Noodle. Kenako Bella ndi Noodle anapita ndi kukaima pafupi ndi Neo, Hope ndi Josh.

Tin anakonzekera kusewera gitala yake ndipo adati, “LOLANI NYIMBO ZIYAMBE!”

Pomwe Tin adaloza Neo ndi Hope, awiriwa anayamba kuwomba ng’oma zawo. Kenako Tin anayamba kuimba, “Phazi lakumanzere kumbuyo,” ndi kuloza ku khamulo.

“Phazi lakumanzere kumbuyo,” khamulo lidayamba kuyimba motero.

Zitatero, Tin adaloza Josh ndiyeyo adayamba kugwedeza mphonda zake mogwirizana ndi kulira kwa nyimbo.

“Phazi lamanja kumbuyo,” adayimba motero Tin.

“Phazi lakumanja kumbuyo,” khamulo lidayamba kuyimbanso motero.

Tin adaloza Bella. Phokoso la zitini linamveka bwino pamene Bella anagwedeza ndi kumenyanisa zitinizo pamodzi. Noodle anafuula mokondwera.

Posakhalitsa phwandolo lidafika pachimake. Pamene Tin anali kuimba nyimbo zake Neo, Josh ndi Bella anali kumenya zida zoimbira. Ndiponso Noodle adali kufuula mokondwera nthawi ndi nthawi!

Kenako oyimba enawo adayimba nyimbo za kudziko lawo. Khamu la anthulo linakuwa mokondwera ndi kuwomba m’manja. Iwo adakonda chiwonetserocho!

“Mwawona,” adatero Tin poyankhula ndi mamembala a We Can Band, “kagulu kakang’ono aka kathandizira kukwaniritsa zomwe zimayembekezereka! Tikukuthokozani inu anayi … kuphatikiza ndi Noodle, aliyense asangalala chifukwa cha phwandoli!”