Mtima wanga dekha
Poti aka sikoyamba kugwa mchikondi
Kumbuka padzana kuti achikondi opanda choona chikondi udali nawo mchikondi
Ndipo achikondi a chabodza chikondi udawapatsa choona chikondi
Koma zonsezi zidakuliza ngati iwe sudali mchikondi
Mchifukwa chake ndikuti dekha mtima wanga izi ndizachikondi
Dekha iwe wanga mtima
Aka sikoyamba kuuzidwa kuti ndiwe wake wapamtima
Kumbukatu yako nambala ankanena pamtima
Ndipo ankati amamva phalombe akakhala pako pamtima
Komatu onsewa anakuswa kumbuka wanga mtima
Choncho dekha usakhale ndi phuma wanga mtima
Usapupulume wanga mtima
Aka sikoyamba kuuzidwa kuti umakondedwa
Kumbuka dzulo dzulo analipo ngati awa okondedwa
Kuti mpaka muyaya sudzasiidwa iwe unauzidwa
Kutiso mpaka kale udzakondedwa unauzidwa
Komatu zonsezi unanamizidwa
Ndipo sichinali chikondi koma kuzuzidwa
Mokupempha dekha mtima wanga
Aka sikoyamba kulonjezedwa ndi wokondedwa
Kumbuka kuti adzakutengera kwawo udzauzidwa
Kutiso zamwano sudzayankhidwa udauzidwa
Nde nanga kwawoko udatengeredwa?
Nanga mwano sukuyankhidwa?
Chonde mtima wanga dekha kuopa kachikena kunamizidwa
Dekha mtima wanga ndagwira mwendo wako
Poti aka sikoyamba kuuzidwa kuti Nyagondwe ndi wako wako
Kumbuka dzulo lija Chepatuma ankati ndi wako wako
Ndipo Nachisare ndi Nyakumwenda adaliso ako ako
Nanga matsuna onsewa akadali ako?
Kodi ziphadzuwa zija ndi azimai aana ako?
Onsewa anakusiya ndiye dekha chonde usamangojijilikapo