Bwerani pano adona chilungamo mulandire
Zomwe ndinene pano zibwana musazitengere
Mwatcheru Mumvetsere kuti apezeke oti kwanu akaonekere
Kodi mmudzi munsemu njonda ndiiti mudaona?
Onse khoma kuwaombetsa mukuti wabwino palibe mumaona
Komatu Mvula yagwa ndipo ndianu maso mwaona
Ndipo dongo lafewa pachulu chakwa Gondwe mutha kukaona
Pitani mukawumbe wanu wabwino mamuna tsiku ndi tsiku muzidzamuona
Pitani wokulupala uja mmafuna mukawumbe kuti mwanu mnyumba azidzagona
Pitani mukawumbe adona mwina ndi zanu zofuna zidzafanana
Mukawumbe wachuma yemwe mumafuna mamuna
Chilichose akakhale nacho poti ena akabwera mumati kapunthabuwe simumufuna
Osanyalanyaza kapena kunyoza kakonzeni chomwe mumafuna
Ngati muli ndi mphwai zakugwirani ndiuzeni dongo ndikatenge
Koma ngati simupita kukawumba cheni cheni mutiuza chomwe mumafuna
Akabwera wamfupi mumati ai wangati chitsa simufuna mamuna
Akabweraso wakuda mumati simumufuna mamuna
Nanji wopanda chuma mmmm mumati zopusa simufuna
Tiziti mumakonda amuna otani adona?
Tiuzeni mwina tifufuze kuti akhale wanu adona
Panda apo kawumbeni nokha dongo ndilowewa
Kuti kawumbeni wanu mamuna mobwereza ndanena ndipo kachikena ndinena
Ndanena ndanena kulikonse mutha kukanena kuti ine chilungamo ndanena
Nanga ndiwe wanji mkazi okana aliyese mamuna?
Susamala kuti ndi mchewa,mtumbuka,mlomwe Kaya Msena
Umafuna otani mamuna oongola wako msana?
Yankhani adona poti kuti aliyese mwamtu wagalu umakana
Kawumbeni wanu wanu oti adzapange zokonda zanu
Eya dongo lafewa kawumbeni wanu mamuna wofewa